Safeguarding

Kudzipereka kwathu pa kuteteza

Ana onse, akulu akulu, mabanja, ndi ma midzi omwe akukumana ndi ife kapena ogwira nafe ntchito (maso ndi maso kapena mu njira za makono) akuyenera kukhala otetezeka, komanso kukhala nafe muzochitika mopanda china chilichonse chowopsya komanso kuchitilidwa nkhanza zina zilizonse.

Timachita chili chonse chothekera kuti ana ndi mabanja awo amve kupatsidwa ulemu ndi kutetezedwa.

Wina aliyense oyimilira bungwe lathu (amenewa ndi akulu akulu oyendetsa bungwe, ogwira ntchito, awo ongodzipereka kugwila ntchito ndife, abwenzi athu pantchito yomwe tikugwirayi) anaphunzitsidwa ndipo ndiwokonzeka kutsatira Ndondomeko za Chitetezo, mu umoyo wazinsinsi zawo komanso wapa ntchito, munthawi ina iliyonse. Izi zimatithandiza ife kukhala ndi makhalidwe apamwamba kwa ana, akulu, mabanja, ndi mmidzi nthawi zonse. Ngati mukuwona kuti izi sizinachitike, kapena makhalidwe komanso zichitochito za oyimilira wa Neotree akukudandaulitsani, tidziwitseni mwachangu.

Makhalidwe ayembekezedwa a onse ogwira ntchito anthu ndi otiyimilira analembedwa momveka bwino mu Ndodomeko zathu za Chitetezo. Sitilora mchitidwe wodyerana masuku pa mutu kapena nkhaza kwa wina aliyense, makamaka ana ndi aakulu apa chiwopsezo. Ngati muli okhudzika za mwana, akulu apa chiwopsezo kapena khalidwe la oyimilira Neotree chonde kaneneni.

Make a donation

Neotree relies on donations and grant funding. We would love your support to roll out the Neotree system to further sites and reduce newborn mortality.